Psalms 99

1Yehova akulamulira,
mitundu ya anthu injenjemere;
Iye wakhala pa mpando wake waufumu, pakati pa akerubi,
dziko lapansi ligwedezeke.
2Mʼziyoni wamkulu ndi Yehova;
Iye ndi wokwezeka pamwamba pa mitundu yonse ya anthu.
3Anthu atamande dzina lanu lalikulu ndi loopsa kwambiri,
Iye ndi woyera.

4Mfumu yamphamvu, iyo imakonda chilungamo
Inu mwakhazikitsa khalidwe losakondera;
mwachita zolungama ndi zoyenera mwa Yakobo.
5Kwezani Yehova Mulungu wathu
ndipo mulambireni pa mapazi ake;
Iye ndi woyera.

6Mose ndi Aaroni anali ena mwa ansembe ake,
Samueli anali pamodzi ndi iwo amene anayitana pa dzina lake;
iwo anayitana Yehova
ndipo Iyeyo anawayankha.
7Iye anayankhula nawo kuchokera mʼchipilala cha mtambo;
iwo anasunga malamulo ake ndi zophunzitsa zomwe anawapatsa.

8Inu Yehova Mulungu wathu,
munawayankha iwo;
Inu kwa Israeli munali Mulungu wokhululuka,
ngakhale munawalanga pa zochita zawo zoyipa.
9Kwezani Yehova Mulungu wathu
ndipo mumulambire pa phiri lake loyera,
pakuti Yehova Mulungu wathu ndi woyera.
Copyright information for NyaCCL